25
Anthu Oyimba Nyimbo 
 1 Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi: 
 2 Kuchokera kwa ana a Asafu: 
Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu. 
 3 Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: 
Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova. 
 4 Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake: 
Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.  5 Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu. 
 6 Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.  7 Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.  8 Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo. 
| 9 Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe, | |
| ana ndi abale ake. | 12 | 
| Maere achiwiri anagwera Gedaliya, | |
| ndi abale ake ndi ana ake. | 12 | 
| 10 Maere achitatu anagwera Zakuri, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 11 Maere achinayi anagwera Iziri, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 12 Maere achisanu anagwera Netaniya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 13 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 14 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 15 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 16 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 17 Maere a khumi anagwera Simei, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 18 Maere a 11 anagwera Azareli, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 19 Maere a 12 anagwera Hasabiya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 20 Maere a 13 anagwera Subaeli, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 21 Maere a 14 anagwera Matitiya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 22 Maere a 15 anagwera Yeremoti, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 23 Maere a 16 anagwera Hananiya, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 24 Maere a 17 anagwera Yosibakasa, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 25 Maere a 18 anagwera Hanani, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 26 Maere a 19 anagwera Maloti, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 27 Maere a 20 anagwera Eliyata, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 28 Maere a 21 anagwera Hotiri, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 29 Maere a 22 anagwera Gidaliti, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 30 Maere a 23 anagwera Mahazioti, | |
| ana ake ndi abale ake. | 12 | 
| 31 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri, | |
| ana ake ndi abale ake | 12. |